8 Adzafanana nao iwo akuwapanga;Ndi onse akuwakhulupirira,
9 Israyeli, khulupirira Yehova:Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao.
10 Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova:Ndiye mthandizi wao, ndi cikopa cao.
11 Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova;Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao.
12 Yehova watikumbukila; adzatidalitsa:Adzadalitsa nyumba ya Israyeli;Adzadalitsa nyumba ya Aroni.
13 Adzadalitsa iwo akuopa Yehova,Ang'ono ndi akuru.
14 Yehova akuonjezereni dalitso, Inu ndi ana anu.