1 Ndimkonda, popeza Yehova amamva,Mau anga ndi kupemba kwanga.
2 Popeza amandicherera khutu lace,Cifukwa cace ndidzaitanira Iye masiku anga onse.
3 Zingwe za imfa zinandizinga,Ndi zowawa za manda zinandigwira:Ndinapeza nsautso ndi cisoni.
4 Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova;Ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga.
5 Yehova ngwa cifundo ndi wolungama;Ndi Mulungu wathu ngwa nsoni.
6 Yehova asunga opusa;Ndidafoka ine, koma anandipulumutsa,
7 Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako;Pakuti Yehova anakucitira cokoma.