6 Yehova asunga opusa;Ndidafoka ine, koma anandipulumutsa,
7 Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako;Pakuti Yehova anakucitira cokoma.
8 Pakuti munalanditsa moyo wanga kuimfa,Maso anga kumisozi, Mapazi anga, ndingagwe.
9 Ndidzayenda pamaso pa Yehova M'dziko la amoyo.
10 Ndinakhulupirira, cifukwa cace ndinalankhula;Ndinazunzika kwambiri.
11 Pofulumizidwa mtima ndinati ine,Anthu Onse nga mabodza.
12 Ndidzabwezera Yehova cianiCifukwa ca zokoma zace zonse anandicitira?