12 Adandizinga ngati njuci;Anazima ngati moto waminga;Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.
13 Kundikankha anandikankha ndikadagwa;Koma Yehova anandithandiza.
14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;Ndipo anakhala cipulumutso canga.
15 M'mahema a olungama muli liu lakupfuula mokondwera ndi la cipulumutso:
16 Dzanja lamanja la Yehova licita mwamphamvu.
17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo,Ndipo ndidzafotokozera nchito za Yehova.
18 Kulanga anandilangadi Yehova:Koma sanandipereka kuimfa ai.