18 Kulanga anandilangadi Yehova:Koma sanandipereka kuimfa ai.
19 Nditsegulireni zipata za cilungamo;Ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova.
20 Cipata ca Yehova ndi ici;Olungama adzalowamo.
21 Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha,Ndipo munakhala cipulumutso canga,
22 Mwala umene omangawo anaukanaWakhala mutu wa pangondya.
23 Ici cidzera kwa Yehova;Ncodabwiza ici pamaso pathu.
24 Tsiku ili ndilo adaliika Yehova;Tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.