20 Cipata ca Yehova ndi ici;Olungama adzalowamo.
21 Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha,Ndipo munakhala cipulumutso canga,
22 Mwala umene omangawo anaukanaWakhala mutu wa pangondya.
23 Ici cidzera kwa Yehova;Ncodabwiza ici pamaso pathu.
24 Tsiku ili ndilo adaliika Yehova;Tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.
25 Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano;Tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.
26 Wodala wakudzayo m'dzina la Yehova;Takudalitsani kocokera m'nyumba ya Yehova.