23 Ici cidzera kwa Yehova;Ncodabwiza ici pamaso pathu.
24 Tsiku ili ndilo adaliika Yehova;Tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.
25 Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano;Tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.
26 Wodala wakudzayo m'dzina la Yehova;Takudalitsani kocokera m'nyumba ya Yehova.
27 Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira;Mangani nsembe ndi zingwe, ku nyanga za guwa la nsembe.
28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;Ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani.
29 Yamikani Yehova, pakuti Iye ndiye wabwino,Pakuti cifundo cace ncosatha.