3 Anene tsono nyumba ya Aroni,Kuti cifundo cace ncosatha.
4 Anene tsono iwo akuopa Yehova,Kuti cifundo cace ncosatha.
5 M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova;Anandiyankha Dandiika motakasuka Yehova.
6 Yehova ndi wanga; sindidzaopa;Adzandicitanji munthu?
7 Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza;M'mwemo ndidzaona cofuna ine pa iwo akundida,
8 Kuthawira kwa Yehova nkokomaKoposa kukhulupirira munthu.
9 Kuthawira kwa Yehova nkokomaKoposa kukhulupirira akulu,