5 M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova;Anandiyankha Dandiika motakasuka Yehova.
6 Yehova ndi wanga; sindidzaopa;Adzandicitanji munthu?
7 Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza;M'mwemo ndidzaona cofuna ine pa iwo akundida,
8 Kuthawira kwa Yehova nkokomaKoposa kukhulupirira munthu.
9 Kuthawira kwa Yehova nkokomaKoposa kukhulupirira akulu,
10 Amitundu onse adandizinga,Zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.
11 Adandizinga, inde, adandizinga:Indedi, m'dzinala Yehova ndidzawaduladula.