101 Ndinaletsa mapazi anga njira iri yonse yoipa,Kuti ndisamalire mau anu.
102 Sindinapatukana nao maweruzo anu;Pakuti Inu munandiphunzitsa.
103 Mau anu azunadi powalawa ine!Koposa uci m'kamwa mwanga.
104 Malangizo anu andizindikiritsa;Cifukwa cace ndidana nao mayendedwe onse acinyengo,
105 Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga,Ndi kuunika kwa panjira panga,
106 Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima,Kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.
107 Ndazunzika kwambiri:Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu.