107 Ndazunzika kwambiri:Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu.
108 Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga,Ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.
109 Moyo wanga ukhala m'dzanja langa cikhalire;Koma sindiiwala cilamulo canu.
110 Oipa anandichera msampha;Koma sindinasokera m'malangizo anu.
111 Ndinalandira mboni zanu zikhale colandira cosatha;Pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.
112 Ndinalingitsa mtima wanga ucite malemba anu,Kosatha, kufikira cimatiziro.
113 Ndidana nao a mitima iwiri;Koma ndikonda cilamulo canu.