109 Moyo wanga ukhala m'dzanja langa cikhalire;Koma sindiiwala cilamulo canu.
110 Oipa anandichera msampha;Koma sindinasokera m'malangizo anu.
111 Ndinalandira mboni zanu zikhale colandira cosatha;Pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.
112 Ndinalingitsa mtima wanga ucite malemba anu,Kosatha, kufikira cimatiziro.
113 Ndidana nao a mitima iwiri;Koma ndikonda cilamulo canu.
114 Inu ndinu pobisalapo panga, ndi cikopa canga;Ndiyembekezera mau anu.
115 Mundicokere ocita zoipa inu;Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.