11 Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga,Kuti ndisalakwire Inu.
12 Inu ndinu wodala Yehova;Ndiphunzitseni malemba anu.
13 Ndinafotokozera ndi milomo yangaMaweruzo onse a pakamwa panu,
14 Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu,Koposa ndi cuma conse,
15 Ndidzalingirira pa malangizo anu,Ndi kupenyerera mayendedwe anu.
16 Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu;Sindidzaiwala mau anu,
17 Mucitire cokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo;Ndipo ndidzasamalira mau anu.