112 Ndinalingitsa mtima wanga ucite malemba anu,Kosatha, kufikira cimatiziro.
113 Ndidana nao a mitima iwiri;Koma ndikonda cilamulo canu.
114 Inu ndinu pobisalapo panga, ndi cikopa canga;Ndiyembekezera mau anu.
115 Mundicokere ocita zoipa inu;Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.
116 Mundicirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo;Ndipo ndisacite manyazi pa ciyembekezo canga.
117 Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa,Ndipo ndidzasamalira malemba anu cisamalire.
118 Mupepulaonseakusokeram'malemba anu;Popeza cinyengo cao ndi bodza.