116 Mundicirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo;Ndipo ndisacite manyazi pa ciyembekezo canga.
117 Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa,Ndipo ndidzasamalira malemba anu cisamalire.
118 Mupepulaonseakusokeram'malemba anu;Popeza cinyengo cao ndi bodza.
119 Mucotsa oipa onse a pa dziko lapansi ngati mphala:Cifukwa cace ndikonda mboni zanu.
120 Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu;Ndipo ndicita mantha nao maweruzo anu.
121 Ndinacita ciweruzo ndi cilungamo;Musandisiyira akundisautsa.
122 Mumkhalire cikole mtumiki wanucimkomere;Odzikuza asandisautse.