121 Ndinacita ciweruzo ndi cilungamo;Musandisiyira akundisautsa.
122 Mumkhalire cikole mtumiki wanucimkomere;Odzikuza asandisautse.
123 Maso anga anatha mphamvu pafuna cipulumutso canu,Ndi mau a cilungamo canu.
124 Mucitire mtumiki wanu monga mwa cifundo canu,Ndipo ndiphunzitseni malemba anu,
125 Ine ndine mtumiki wanu, ndizindikiritseni;Kuti ndidziwe mboni zanu.
126 Yafika nyengo yakuti Yehova acite kanthu;Pakuti anaswa cilamulo canu.
127 Cifukwa cace ndikonda malamulo anuKoposa golidi, Inde golidi woyengeka,