127 Cifukwa cace ndikonda malamulo anuKoposa golidi, Inde golidi woyengeka,
128 Cifukwa cace ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse;Koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.
129 Mboni zanu nzodabwiza; Cifukwa cace moyo wanga uzisunga,
130 Potsegulira mau anu paunikira;Kuzindikiritsa opusa.
131 Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefu wefu;Popeza ndinakhumba malamulo anu.
132 Munditembenukire, ndi kundicitira cifundo,Monga mumatero nao akukonda dzina lanu.
133 Kfiazikitsanimapaziangam'mau anu;Ndipo zisandigonjetse zopanda pace ziri zonse.