129 Mboni zanu nzodabwiza; Cifukwa cace moyo wanga uzisunga,
130 Potsegulira mau anu paunikira;Kuzindikiritsa opusa.
131 Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefu wefu;Popeza ndinakhumba malamulo anu.
132 Munditembenukire, ndi kundicitira cifundo,Monga mumatero nao akukonda dzina lanu.
133 Kfiazikitsanimapaziangam'mau anu;Ndipo zisandigonjetse zopanda pace ziri zonse.
134 Mundiombole ku nsautso ya munthu:Ndipo ndidzasamalira malangizo anu.
135 Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu;Ndipo mundiphunzitse malemba anu.