140 Mau anu ngoyera ndithu;Ndi mtumiki wanu awakonda.
141 Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa;Koma sindiiwala malemba anu.
142 Cilungamo canu ndico cilungamo cosatha;Ndi cilamulo canu ndico coonadi.
143 Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera;Koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.
144 Mboni zanu ndizo zolungama kosatha;Mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.
145 Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova;Ndidzasunga malemba anu.
146 Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni,Ndipo ndidzasamalira mboni zanu.