149 Imvani liu langa monga mwa cifundo canu;Mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.
150 Otsata zaciwembu andiyandikira;Akhala kutali ndi cilamulo canu.
151 Inu muli pafupi, Yehova;Ndipo malamulo anu onse ndiwo coonadi,
152 Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu,Kuti munazikhazika kosatha,
153 Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse;Pakuti sindiiwala cilamulo canu.
154 Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole;Mundipatse moyo monga mwa mau anu.
155 Cipulumutso citalikira oipa;Popeza safuna malemba anu.