164 Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi,Cifukwa ca maweruzo anu alungama.
165 Akukonda cilamulo canu ali nao mtendere wambiri;Ndipo alibe cokhumudwitsa.
166 Ndinayembekeza cipulumutso canu, Yehova,Ndipo ndinacita malamulo anu.
167 Moyo wanga unasamalira mboni zanu;Ndipo ndizikonda kwambiri.
168 Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu;Popeza njira zanga zonse ziri pamaso panu,
169 Kupfuula kwanga kuyandikire pamaso pano, Yehova;Mundizindikiritse monga mwa mau anu.
170 Kupemba kwanga kudze pamaso panu;Mundilanditse monga mwa mau anu.