169 Kupfuula kwanga kuyandikire pamaso pano, Yehova;Mundizindikiritse monga mwa mau anu.
170 Kupemba kwanga kudze pamaso panu;Mundilanditse monga mwa mau anu.
171 Milomo yanga iturutse cilemekezo;Popeza mundiphunzitsa malemba anu.
172 Lilime langa liyimbire mau anu;Pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.
173 Dzanja lanu likhale lakundithandizaPopezandinasankha malangizo anu.
174 Ndinakhumba cipulumutso canu, Yehova;Ndipo cilamulo canu ndico condikondweretsa.
175 Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani;Ndipo maweruzo anu andithandize.