18 Munditsegulire maso, kuti ndipenyeZodabwiza za m'cilamulo canu.
19 Ine ndine mlendo pa dziko lapansi;Musandibisire malamulo anu.
20 Mtima wanga wasweka ndi kukhumbaMaweruzo anu nyengo zonse.
21 Munadzudzula odzikuza otembereredwa,Iwo akusokera kusiyana nao malamulo anu.
22 Mundicotsere cotonza, ndi cimpepulo;Pakuti ndinasunga mboni zanu.
23 Nduna zomwe zinakhala zondineneza;Koma mtumiki wanu analingirira malemba anu.
24 Mboni zanu zomwe ndizo zondikondwetsa,Ndizo zondipangira nzeru.