2 Odala iwo akusunga mboni zace,Akumfuna ndi mtima wonse;
3 Inde, sacita cosalungama;Ayenda m'njira zace.
4 Inu munatilamulira.Tisamalire malangizo anu ndi cangu,
5 Ha! mwenzi zitakhazikika njira zangaKuti ndisamalire malemba anu.
6 Pamenepo sindidzacita manyazi,Pakupenyerera malamulo anu onse.
7 Ndidzakuyanrikani ndi mtima woongoka,Pakuphunzira maweruzo anu olungama.
8 Ndidzasamalira malemba anu:Musandisiye ndithu.