22 Mundicotsere cotonza, ndi cimpepulo;Pakuti ndinasunga mboni zanu.
23 Nduna zomwe zinakhala zondineneza;Koma mtumiki wanu analingirira malemba anu.
24 Mboni zanu zomwe ndizo zondikondwetsa,Ndizo zondipangira nzeru.
25 Moyo wanga umamatika ndi pfumbi;Mundipatse moyo monga mwa mau anu.
26 Ndinafotokozera njira zanga, ndipo munandiyankha:Mundiphunzitse malemba anu.
27 Mundizindikiritse njira ya malangizo anu;Kuti ndilingalire zodabwiza zanu.
28 Moyo wanga wasungunuka ndi cisoni:Mundilimbitse monga mwa mau anu.