27 Mundizindikiritse njira ya malangizo anu;Kuti ndilingalire zodabwiza zanu.
28 Moyo wanga wasungunuka ndi cisoni:Mundilimbitse monga mwa mau anu.
29 Mundicotsere njira ya cinyengo;Nimundipatse mwacifundo cilamulo canu.
30 Ndinasankha njira yokhulupirika;Ndinaika maweruzo anu pamaso, panga,
31 Ndimamatika nazo mboni zanu;Musandicititse manyazi, Yehova.
32 Ndidzathamangira njira ya malamulo anu,Mutakulitsa mtima wanga.
33 Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu;Ndidzaisunga kufikira kutha kwace.