38 Limbitsirani mtumiki wanu mau anu,Ndiye wodzipereka kukuopani.
39 Mundipatutsire cotonza canga ndiciopaco;Popeza maweruzo anu ndi okoma.
40 Taonani, ndinalira malangizo anu;Mundipatse moyo mwa cilungamo canu.
41 Ndipo cifundo canu cindidzere, Yehova,Ndi cipulumutso canu, monga mwa mau anu.
42 Kuti ndikhale nao mau akuyankha wonditonza;Popeza ndikhulupirira mau anu.
43 Ndipo musandicotsere ndithu mau a coonadi pakamwa panga;Pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.
44 Potero ndidzasamalira malamulo anu cisamalireKu nthawi za nthawi.