4 Inu munatilamulira.Tisamalire malangizo anu ndi cangu,
5 Ha! mwenzi zitakhazikika njira zangaKuti ndisamalire malemba anu.
6 Pamenepo sindidzacita manyazi,Pakupenyerera malamulo anu onse.
7 Ndidzakuyanrikani ndi mtima woongoka,Pakuphunzira maweruzo anu olungama.
8 Ndidzasamalira malemba anu:Musandisiye ndithu.
9 Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ace bwanji?Akawasamalira monga mwa mau anu.
10 Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse;Ndisasokere kusiyana nao malamulo anu.