41 Ndipo cifundo canu cindidzere, Yehova,Ndi cipulumutso canu, monga mwa mau anu.
42 Kuti ndikhale nao mau akuyankha wonditonza;Popeza ndikhulupirira mau anu.
43 Ndipo musandicotsere ndithu mau a coonadi pakamwa panga;Pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.
44 Potero ndidzasamalira malamulo anu cisamalireKu nthawi za nthawi.
45 Ndipo ndidzayenda mwaufulu;Popeza ndinafuna malangizo anu.
46 Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu,Osacitapo manyazi.
47 Ndipo ndidzadzikondweretsa nao malamulo anu,Amene ndiwakonda.