48 Ndidzakwezanso manja anga ku malamulo anu, amene ndiwakonda;Ndipo ndidzalingalira pa malemba anu.
49 Kumbukilani mau a kwa mtumiki wanu,Amene munandiyembekezetsa nao.
50 Citonthozo canga m'kuzunzika kwanga ndi ici;Pakuti mau anu anandipatsa moyo.
51 Odzikuza anandinyoza kwambiri:Koma sindinapatukanso naco cilamulo canu.
52 Ndinakumbukila maweruzo anu kuyambira kale, Yehova,Ndipo ndinadzitonthoza.
53 Ndinasumwa kwakukuru,Cifukwa ca oipa akusiya cilamulo canu.
54 Malemba anu anakhala nyimbo zangaM'nyumba ya ulendo wanga,