54 Malemba anu anakhala nyimbo zangaM'nyumba ya ulendo wanga,
55 Usiku ndinakumbukila dzina lanu, Yehova,Ndipo ndinasamalira cilamulo canu.
56 Ici ndinali naco,Popeza ndinasunga malangizo anu.
57 Yehova ndiye gawo langa:Ndinati ndidzasunga mau anu.
58 Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse:Mundicitire cifundo monga mwa mau anu.
59 Ndinaganizira njira zanga,Ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu.
60 Ndinafulumira, osacedwa,Kusamalira malamulo anu.