56 Ici ndinali naco,Popeza ndinasunga malangizo anu.
57 Yehova ndiye gawo langa:Ndinati ndidzasunga mau anu.
58 Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse:Mundicitire cifundo monga mwa mau anu.
59 Ndinaganizira njira zanga,Ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu.
60 Ndinafulumira, osacedwa,Kusamalira malamulo anu.
61 Anandikulunga nazo zingwe za oipa;Koma sindinaiwala cilamulo canu.
62 Pakati pa usiku ndidzauka kukuyamikaniCifukwa ca maweruzo anu olungama.