62 Pakati pa usiku ndidzauka kukuyamikaniCifukwa ca maweruzo anu olungama.
63 Ine ndine wakuyanjana nao onse akukuopani,Ndi iwo akusamalira malangizo anu.
64 Dziko lapansi lidzala naco cifundo canu, Yehova;Mundiphunzitse malemba anu.
65 Munacitira mtumiki wanu cokoma, Yehova,Monga mwa mau anu.
66 Mundiphunzitse cisiyanitso ndi nzeru;Pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.
67 Ndisanazunzidwe ndinasokera; Koma tsopano ndisamalira mau anu.
68 Inu ndinu wabwino, ndi wakucita zabwino;Mundiphunzitse malemba anu.