64 Dziko lapansi lidzala naco cifundo canu, Yehova;Mundiphunzitse malemba anu.
65 Munacitira mtumiki wanu cokoma, Yehova,Monga mwa mau anu.
66 Mundiphunzitse cisiyanitso ndi nzeru;Pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.
67 Ndisanazunzidwe ndinasokera; Koma tsopano ndisamalira mau anu.
68 Inu ndinu wabwino, ndi wakucita zabwino;Mundiphunzitse malemba anu.
69 Odzikuza anandipangira bodza:Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.
70 Mtima wao unona ngati mafuta;Koma ine ndikondwera naco cilamulo canu.