67 Ndisanazunzidwe ndinasokera; Koma tsopano ndisamalira mau anu.
68 Inu ndinu wabwino, ndi wakucita zabwino;Mundiphunzitse malemba anu.
69 Odzikuza anandipangira bodza:Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.
70 Mtima wao unona ngati mafuta;Koma ine ndikondwera naco cilamulo canu.
71 Kundikomera kuti ndinazunzidwa;Kuti ndiphunzire malemba anu.
72 Cilamulo ca pakamwa panu cindikomeraKoposa golidi ndi siliva zikwi zikwi.
73 Manja anu anandilenga nandiumba;Mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.