70 Mtima wao unona ngati mafuta;Koma ine ndikondwera naco cilamulo canu.
71 Kundikomera kuti ndinazunzidwa;Kuti ndiphunzire malemba anu.
72 Cilamulo ca pakamwa panu cindikomeraKoposa golidi ndi siliva zikwi zikwi.
73 Manja anu anandilenga nandiumba;Mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.
74 Iwo amene akuopani adzandiona ine nadzakondwera;Popeza ndayembekezera mau anu;
75 Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova,Ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.
76 Cifundo canu cikhaletu cakunditonthoza, ndikupemphani,Monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.