78 Odzikuza acite manyazi, popeza anandicitira monyenga ndi bodza:Koma ine ndidzalingalira malangizo anu.
79 Iwo akuopa Inu abwere kwa ine,Ndipo adzadziwa mboni zanu.
80 Mtima wanga ukhale wangwiro m'malemba anu;Kuti ndisacite manyazi.
81 Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba cipulumutso canu:Ndinayembekezera mau anu.
82 Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu,Ndikuti, Mudzanditonthoza liti?
83 Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira;Koma sindiiwala malemba anu.
84 Masiku a mtumiki wanu ndiwo angati?Mudzaweruza liti iwo akundilondola koipa?