80 Mtima wanga ukhale wangwiro m'malemba anu;Kuti ndisacite manyazi.
81 Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba cipulumutso canu:Ndinayembekezera mau anu.
82 Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu,Ndikuti, Mudzanditonthoza liti?
83 Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira;Koma sindiiwala malemba anu.
84 Masiku a mtumiki wanu ndiwo angati?Mudzaweruza liti iwo akundilondola koipa?
85 Odzikuza anandikumbira mbuna,Ndiwo osasamalira cilamulo canu.
86 Malamulo anu onse ngokhulupirika;Andilondola nalo bodza; ndithandizeni.