83 Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira;Koma sindiiwala malemba anu.
84 Masiku a mtumiki wanu ndiwo angati?Mudzaweruza liti iwo akundilondola koipa?
85 Odzikuza anandikumbira mbuna,Ndiwo osasamalira cilamulo canu.
86 Malamulo anu onse ngokhulupirika;Andilondola nalo bodza; ndithandizeni.
87 Akadandithera pa dziko lapansi; Koma ine sindinasiya malangizo anu.
88 Mundipatse moyo monga mwa cifundo canu;Ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu,
89 Mau anu aikika kumwamba,Kosatha, Yehova.