92 Cilamulo canu cikadapanda kukhala cikondweretso canga,Ndikadatayika m'kuzunzika kwanga.
93 Sindidzaiwala malangizo anu nthawi zonse;Popeza munandipatsa nao moyo.
94 Ine ndine wanu, ndipulumutseniPakuti ndinafuna malangizo anu.
95 Oipa anandilalira kundiononga;Koma ndizindikira mboni zanu.
96 Ndinapenya malekezero ace a ungwiro wonse;Koma lamulo lanu ndi lotakasuka ndithu.
97 Ha! Ndikondadi cilamulo canu;Ndilingiriramo ine tsiku lonse.
98 Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga;Pakuti akhala nane cikhalire.