99 Ndiri nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse;Pakuti ndilingalira mboni zanu.
100 Ndizindikira koposa okalambaPopeza ndinasunga malangizo anu.
101 Ndinaletsa mapazi anga njira iri yonse yoipa,Kuti ndisamalire mau anu.
102 Sindinapatukana nao maweruzo anu;Pakuti Inu munandiphunzitsa.
103 Mau anu azunadi powalawa ine!Koposa uci m'kamwa mwanga.
104 Malangizo anu andizindikiritsa;Cifukwa cace ndidana nao mayendedwe onse acinyengo,
105 Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga,Ndi kuunika kwa panjira panga,