1 Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa;Pakuti okhulupirika acepa mwa ana a anthu.
2 Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wace:Amanena ndi mlomo wotyasika, ndi mitima iwiri.
3 Yehova adzadula milomo yonse yotyasika,Lilime lakudzitamandira:
4 Amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa;Milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?