1 Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa;Pakuti okhulupirika acepa mwa ana a anthu.
2 Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wace:Amanena ndi mlomo wotyasika, ndi mitima iwiri.
3 Yehova adzadula milomo yonse yotyasika,Lilime lakudzitamandira:
4 Amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa;Milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?
5 Cifukwa ca kupasuka kwa ozunzika, cifukwa ca kuusa moyo kwa aumphawi,Ndiuka tsopano, ati Yehova; Ndidzamlonga mosungika muja alaka-lakamo.
6 Mau a Yehova ndi mau oona;Ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi,Yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.