5 Cifukwa ca kupasuka kwa ozunzika, cifukwa ca kuusa moyo kwa aumphawi,Ndiuka tsopano, ati Yehova; Ndidzamlonga mosungika muja alaka-lakamo.
6 Mau a Yehova ndi mau oona;Ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi,Yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.
7 Mudzawasunga, Yehova,Mudzawacinjirizira mbadwo uno ku nthawi zonse.
8 Oipa amayenda mozungulira-zungulira,Potamanda iwo conyansa mwa ana a anthu.