5 Yehova ndiye wakukusunga;Yehova ndiye mthunzi wako wa ku dzanja lako lamanja.
6 Dzuwa silidzawamba usana,Mwezi sudzakupanda usiku.
7 Yehova adzakusunga kukucotsera zoipa ziri zonse;Adzasunga moyo wako.
8 Yehova adzasungira kuturuka kwako ndi kulowa kwako,Kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.