1 Ndinakondwera m'mene ananena nane,Tiyeni ku nyumba ya Yehova.
2 Mapazi athu alinkuima M'zipata zanu, Yerusalemu.
3 Yerusalemu anamangidwaNgati mudzi woundana bwino:
4 Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova;Akhale mboni ya kwa Israyeli,Ayamike dzina la Yehova.
5 Pakuti pamenepo anaika mipando ya ciweruzo,Mipando ya nyumba ya Davide.
6 Mupempherere mtendere wa Yerusalemu;Akukonda inu adzaona phindu.