3 Yerusalemu anamangidwaNgati mudzi woundana bwino:
4 Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova;Akhale mboni ya kwa Israyeli,Ayamike dzina la Yehova.
5 Pakuti pamenepo anaika mipando ya ciweruzo,Mipando ya nyumba ya Davide.
6 Mupempherere mtendere wa Yerusalemu;Akukonda inu adzaona phindu.
7 M'linga mwako mukhale mtendere,M'nyumba za mafumu mukhale phindu.
8 Cifukwa ca abale anga ndi mabwenzi anga,Ndidzanena tsopano, Mukhale mtendere mwa inu.
9 Cifukwa ca nyumba ya Yehova Mulungu wathuNdidzakufunira zokoma,