1 Akadapanda kukhala nafe Yehova,Anene tsono Israyeli;
2 Akadapanda kukhala nafe Yehova,Pakutiukira anthu:
3 Akadatimeza amoyo,Potipsera mtima wao.
4 Akadatimiza madziwo,Mtsinje ukadapita pa moyo wathu;
5 Madzi odzikuza akadapita pa moyo wathu.