1 Akadapanda kukhala nafe Yehova,Anene tsono Israyeli;
2 Akadapanda kukhala nafe Yehova,Pakutiukira anthu:
3 Akadatimeza amoyo,Potipsera mtima wao.
4 Akadatimiza madziwo,Mtsinje ukadapita pa moyo wathu;
5 Madzi odzikuza akadapita pa moyo wathu.
6 Alemekezedwe Yehova,Amene sanatipereka kumano kwao tikhale cakudya cao.
7 Moyo wathu unaonjoka ngati mbalame mu msampha wa msodzi;Msampha unatyoka ndi ife tinaonioka.