2 Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka,Ndi lilime lathu linapfuula mokondwera;Pamenepo anati mwa amitundu,Yehova anawacitira iwo zazikuru,
3 Yehova anaticitira ife zazikuru;Potero tikhala okondwera.
4 Bwezani ukapolo wathu, Yehova,Ngati mitsinje ya ku Mwera.
5 Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kupfuula mokondwera.
6 Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa;Adzabweranso ndithu ndi kupfuula mokondwera, alikunyamula mitolo yace.